Child Rights Information and Documentation Centre
Child Rights Malawi : AECL Malawi
Child Rights CRIDOC About CRIDOC Contact Us SiteMap
Ma bungwe odziyimira pawokha ku Malawi

Kusintha Achinyamata Otoreza Kuntaya kuti Akhale Ophunzira kapena odziwa nthito zosiyana...

Bungwe la CRIDOC ndi la NYCOM Asayanira Mgwirizano Wofalitsa Polujekitiyi

Click to enlarge photo

Umu ndi m'mene achinyamatawa amatolezera kuntaya. Apa akukwera galimoto ya City yomwe imataya zinyalala kuntayaku.

Dinani apa kuti muwone zithunzi zambiri »

Bingwe la National Youth Council of Malawi (NYCOM), ndithandizo lochokera ku Kellog foundation, likuyendetsa pulojekiti ya zaka ziwiri yomwe ithandize achinyamata amene amapezekapezeka ku malo otayirako zinyalala mumizinda ikuluikulu iwiri ya Lilongwe and Blantyre. Bungwe la CRIDOC linasayinirana mgwirizano ndi bungwe la NYCOM kuti lithandizepo pofalitsa pa wailesi ya kanema, ya radio, kapena kulemba mu nyuzipepala m'mene pulojekitiyi ikuthandizira achinyamatawa. Ma pulogalamuwa akuwulutsidwa pa MBC Radio 1 komanso pa TVM.

Werengani zambiri za pulojekitiyi apa»  

Mverani zomwe a CRIDOC adajambula apa»

Wonerani zomwe a CRIDOC adajambula apa»

Bookmark and Share

CRIDOC Ikhazikitsa Malo Owerengera Mabuku ndi Zina Zosiyanasiyana

Click to enlarge photo

Pofuna kukwaniritsa bwino zina za zolinga zathu, ife a CRIDOC takhazikitsa malo omwe mungapeze zinthu kapena zipangizo zosiyanasiyana zophunzitsira ma ufulu a wana ndi nkhani zachitukuko. Malowa amatchedwa kuti "Resource centre" kapena "Library".

Ena mwa anthu amene akugwiritsa ntchito malowa ndi ana a sukulu, ogwra nthito ku mabungwe oyima pawokha, ndi ena otero. Koma kuti ife tikuloreni kugwiritsa nthito malowa, mukuyenera kuti mukhale kaye membela. Choncho, mukuyenera kutenga ma fomu (application forms).
Pezani ma fomu apa »

Dziwani za kukhazikitsa kwa Ndondomeko za Muphuziro Zatsopano

CRIDOC, yomwe ndi membala wa ma bungwe omwe si aboma amene amaona zamaphunziro mu Malawi muno lotchedwa Civil Society Coalition for Quality Basic Education (CSCQBE), linali nawo mu komiti (taskforce) yomwe yakhazikhitsa ndondomeko ya maphunziro.

Ndondomekoyi, yomwe ikutchedwa "Education manifesto/Agenda" cholinga chake ndikuunikira zinthu zimene boma ndi mabungwe ena ayenera kutsata kupititsa maphunziro patsogola, makamaka nthawi ino yomwe dziko la Malawi lachita masankho a Pulezidenti ndi aphungu akunyumba ya malamulo mu mwezi wa Meyi 2009. Bungwe la CSCQBE likhala likukambirana ndi anthu komanso zipani zosiyanasiyana za ndale pankhani yamaphunziro.
Werengani zambiri apa»
Werengani bukuli/ndondomekoyi apa»

Cridoc Ndi Maiko Amu Africa Alimbana Ndi Mchitidwe Wochita Zoipa Ndi Wana

Apa atsikana awiri a CRIDOC (akhala kumanzere) akucheza ndi anzawo ochokera mayiko ena

Oyimirira anayi a CRIDOC anali nawo pa msonkhano wa maiko pafupi-fupi khumi (10) posachedwapa mu mzinda wa Dar-Es-Salaam mu dziko la Tanzania ndicholinga kuunikanso momwe maikowa angalimbikitsire ntchito zolimbana ndi mchitidwe wankhanza ndi kugwilitsa ntchito ana munjira zachiwerewere. Bungwe lalikulu lomwe lamaona njira zothetsera mchitidwewu padziko lonse lapansi lomwe limatchedwa End Child Prostitution, Child Pornography and Trafficking of Children for Sexual Purposes (ECPAT) ndi limene lidapangitsa msonkhanowu.

Werengani Zambiri Apa»

 

 
TakingITGlobal - Inspire. Inform. Involve.

Kudziwa za CRIDOC | Ntchito za CRIDOC | Mungatipeze Bwanji | Njira Zopezera Chithandizo

Child Rights Information & Documentation Centre, Msandula House, Behind Immigration Dept,
P.O. Box X204, Post Dot Net, Crossroads, Lilongwe, Malawi
Tel: +265 1 750 098 Fax: +265 1 750 058
E-mail:
info@cridoc.net Website: www.cridoc.net

© 2009 cridoc.net. All rights reserved
Website Designed by First Web Foundation